Micah 1:11 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Inu anthu a ku Safiri mudzapita ku ukapolo muli maliseche ndi amanyazi. Anthu a ku Zanani satuluka mu mzinda wao. Mukamva anthu a ku Betezele akulira, mudzadziŵa kuti sangathe kukuthandizani.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pitiratu, wokhala m'Safiri iwe, wamaliseche ndi wamanyazi; wokhala m'Zanani sanatuluke; maliro a Betezele adzakulandani pokhala pake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Inu anthu okhala ku Safiro, muzipita ku ukapolo muli amaliseche ndi amanyazi. Iwo amene akukhala ku Zanaani sadzatuluka. Beti-Ezeli akulira mwachisoni; chitetezo chake chakuchokerani.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pitiratu, wokhala m'Safiri iwe, wamarisece ndi wamanyazi; wokhala m'Zanana sanaturuka; maliro a Betezeli adzakulandani pokhala pace.