Micah 1:12 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Anthu a ku Maroti ali ndi nkhaŵa poyembekeza thandizo, chifukwa Chauta wadzetsa chiwonongeko pafupi ndi Yerusalemu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti wokhala m'Maroti alindira chokoma, popeza choipa chatsika kwa Yehova kunka kuchipata cha Yerusalemu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anthu amene amakhala ku Maroti akubuwula ndi ululu, akuyembekezera thandizo, chifukwa Yehova wabweretsa tsoka, lafika mpaka pa chipata cha Yerusalemu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti wokhala m'Maroti alindira cokoma, popeza coipa catsika kwa Yehova kumka ku cipata ca Yerusalemu.