Micah 1:13 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mangani akavalo ku magaleta, inu anthu a ku Lakisi. Mudatsanzira machimo a Israele, potero mudachimwitsa anthu a ku Ziyoni.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Manga galeta kukavalo waliwiro, wokhala m'Lakisi iwe, woyamba kuchimwitsa mwana wamkazi wa Ziyoni ndi iye; pakuti zolakwa za Israele zinapezedwa mwa iwe.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Inu anthu okhala ku Lakisi mangani akavalo ku magaleta. Inu amene munayamba kuchimwitsa mwana wamkazi wa Ziyoni, pakuti zolakwa za Israeli zinapezeka pakati panu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Manga gareta ku kavalo waliwiro, wokhala m'Lakisi iwe, woyamba kucimwitsa mwana wamkazi wa Ziyoni ndi iye; pakuti zolakwa za Israyeli zinapezedwa mwa iwe.