Micah 1:16 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Inu a ku Yuda, metani mpala, kuwonetsa kuti mukulira ana anu amene munkaŵakonda. Mukhale ndi dazi la dembo poti anawo adakusiyani, adatengedwa ku ukapolo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Udziyeseze wadazi, udzimete wekha chifukwa cha ana ako okondwera nao; kuza dazi lako ngati la muimba; pakuti anakuchokera, nalowa ndende.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Metani mipala mitu yanu kuonetsa kuti mukulirira ana anu amene mumawakonda; mudzichititse dazi ngati dembo, pakuti anawo adzatengedwa pakati panu kupita ku ukapolo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Udziyeseze wadazi, udzimete wekha cifukwa ca ana ako okondwera nao; kuza dazi lako ngati la muimba; pakuti anakucokera, nalowa ndende.