Micah 1:7 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mafano ake onse ndidzaŵaphwanyaphwanya, ndipo mitulo yake yonse idzatenthedwa m'moto. Zithunzi zonse za milungu yake ndidzaziwononga. Mphatso zake adazilandira kuchokera ku malipiro a akazi adama, choncho enanso adzazigwiritsa ntchito ngati malipiro a akazi adama.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndi mafano ake osema onse adzaphwanyika, ndi mphotho zake zonse zidzatenthedwa ndi moto, ndi mafano ake onse ndidzawapasula; pakuti anazisonkhanitsa pa mphotho ya mkazi wachiwerewere, ndipo zidzabwerera kumphotho ya mkazi wachiwerewere.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mafano ake onse ndidzawaphwanyaphwanya; mphatso zake zonse ndidzazitentha ndi moto; ndidzawononga zifanizo zonse za milungu yake. Popeza analandira mphatso zake kuchokera ku malipiro a akazi achiwerewere, mphatsozonso zidzagwiritsidwa ntchito ndi ena ngati malipiro a akazi achiwerewere.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndi mafano ace osema onse adzaphwanyika, ndi mphotho zace zonse zidzatenthedwa ndi moto, ndi mafano ace onse ndidzawapasula; pakuti anazisonkhanitsa pa mphotho ya mkazi waciwerewere, ndipo zidzabwerera ku mphotho ya mkazi waciwerewere.