Micah 1:8 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Mika adati, “Nchifukwa chake ndidzalira komvetsa chisoni. Ndidzayenda maliseche, ndidzakuwa ngati nkhandwe ndi kulira ngati nthiŵatiŵa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chifukwa cha ichi ndidzachita maliro, ndi kuchema, ndidzayenda wolandidwa ndi wamaliseche; ndidzalira ngati nkhandwe, ndi kubuma ngati nthiwatiwa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Chifukwa cha zimenezi ine ndidzalira momvetsa chisoni; ndidzayenda wopanda nsapato ndi wamaliseche. Ndidzafuwula ngati nkhandwe ndi kulira ngati kadzidzi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cifukwa ca ici ndidzacita maliro, ndi kucema, ndidzayenda wolandidwa ndi wamarisece; ndidzalira ngati mimbulu, ndi kubuma ngati nthiwatiwa.