Micah 2:1 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsoka kwa anthu amene amakonzekera chiwembu, amene usiku wonse amalingalira ntchito zoipa. Akadzuka m'maŵa amakazichitadi, pakuti mphamvu zake ali nazo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Tsoka iwo akulingirira chinyengo, ndi kukonza choipa pakama pao! Kutacha m'mawa achichita, popeza chikhozeka m'manja mwao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsoka kwa amene amakonzekera chiwembu, kwa amene amakonzekera kuchita zoyipa usiku pa mabedi awo! Kukacha mmawa amakachitadi chifukwa ali ndi mphamvu zochitira zimenezo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Tsoka iwo akulingirira cinyengo, ndi kukonza coipa pakama pao! kutaca m'mawa acicita, popeza cikhozeka m'manja mwao.