Micah 2:11 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Munthu wina atamapita uku ndi uku akulalika zabodza kuti, ‘Ndithudi mudzakhala ndi vinyo ndi zakumwa zamphamvu zambiri,’ mlaliki wotere ndi amene anthu aŵa angamkonde.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Munthu akayenda ndi mtima wachinyengo ndi kunama, ndi kuti, Ndidzanenera kwa iwe za vinyo ndi chakumwa chakuledzeretsa; iye ndiye mneneri wa anthu ake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ngati munthu wabodza ndi wachinyengo abwera nʼkunena kuti, ‘Ine ndidzanenera ndipo mudzakhala ndi vinyo ndi mowa wambiri, woteroyo adzakhala mneneri amene anthu awa angamukonde!’
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Munthu akayenda ndi mtima wacinyengo ndi kunama, ndi kuti, Ndidzanenera kwa iwe za vinyo ndi cakumwa cakuledzeretsa; iye ndiye mneneri wa anthu ace.