Micah 2:12 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Koma inu banja lonse la Yakobe, ndidzakusonkhanitsani. Onse otsala a ku Israele ndidzaŵasonkhanitsa pamodzi ngati nkhosa m'khola, ngati gulu la zoŵeta pa busa lake. Malowo adzakhala thithithi ndi chinamtindi cha anthu.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndidzakumemezani ndithu, Yakobo, inu nonse; ndidzasonkhanitsa ndithu otsala a Israele; ndidzawaika pamodzi ngati nkhosa za ku Bozira; ngati zoweta pakati pa busa pao adzachita phokoso chifukwa cha kuchuluka anthu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Inu banja la Yakobo, ndidzakusonkhanitsani nonse; ndidzawasonkhanitsa pamodzi otsala a ku Israeli. Ndidzawabweretsa pamodzi ngati nkhosa mʼkhola, ngati ziweto pa msipu wake; malowo adzadzaza ndi chinamtindi cha anthu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndidzakumemezani ndithu, Yakobo, inu nonse; ndidzasonkhanitsa ndithu otsala a Israyeli; ndidzawaika pamodzi ngati nkhosa za ku Boma; ngati zoweta pakati pa busa pao adzacita phokoso cifukwa ca kucuruka anthu.