Micah 2:4 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsiku limenelo anthu adzakupekerani nthano yokunyodolani, adzakuimbani nyimbo yamaliro, adzati, ‘Taonongeka kotheratu. Dziko limene Chauta adatigaŵira, bwanji afuna kutilanda! Minda yathu aigaŵira amene atigwira ukapolo.’ ”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Tsiku ilo adzanena fanizo lakunena inu, nadzalira maliro olemerera, ndi kuti, Tapasuka konse; iye asintha gawo la anthu anga; ha! Andichotsera ili! Agawira opikisana minda yathu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsiku limenelo anthu adzakuchitani chipongwe; adzakunyogodolani ndi nyimbo iyi yamaliro: ‘Tawonongeka kotheratu; dziko la anthu anga lagawidwa. Iye wandilanda! Wapereka minda yathu kwa anthu otiwukira.’ ”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Tsiku ilo adzanena fanizo lakunena inu, nadzalira maliro olemerera, ndi kuti, Tapasuka konse; iye asintha gawo la anthu anga; ha! andicotsera ili! agawira opikisana minda yathu.