Micah 2:8 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chauta akuti, “Koma inu mumaukira anthu anga ngati mdani. Mumaŵavula mkanjo anthu amtendere, amene amangoyenda ndi mtima wokhazikika, osaganizako za nkhondo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma ngakhale dzulo anthu anga anauka ngati mdani; mukwatula chofunda kumalaya a iwo opitirira mosatekeseka, ngati anthu osafuna nkhondo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Posachedwapa anthu anga andiwukira ngati mdani. Mumawavula mkanjo wamtengowapatali anthu amene amadutsa mosaopa kanthu, monga anthu amene akubwera ku nkhondo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma ngakhale dzulo anthu anga anauka ngati mdani; mukwatula copfunda ku maraya a iwo opitirira mosatekeseka, ngati anthu osafuna nkhondo.