Micah 3:11 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Atsogoleri ake saweruza popanda chiphuphu, ansembe ake saphunzitsa popanda malipiro, aneneri ake salosa popanda ndalama. Komabe amagonera pa Chauta ndi kunena kuti, “Kodi suja Chauta ali pakati pathu? Tsoka silingatigwere ai.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Akulu ake aweruza chifukwa cha mphotho, ndi ansembe ake aphunzitsa chifukwa cha malipo, ndi aneneri ake alosa chifukwa cha ndalama; koma atsamira pa Yehova, nati, Kodi Yehova sali pakati pa ife? Palibe choipa chodzatigwera.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Atsogoleri ake amalandira chiphuphu kuti aweruze, ansembe ake amalandira malipiro kuti alalikire, ndipo aneneri ake amanenera kuti alandire ndalama. Komatu amatsamira pa Yehova nʼkumanena kuti, “Kodi Yehova sali pakati pathu? Palibe tsoka limene lidzatigwere.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Akuru ace aweruza cifukwa ca mphotho, ndi ansembe ace aphunzitsa cifukwa ca malipo, ndi aneneri ace alosa cifukwa ca ndarama; koma atsamira pa Yehova, nati, Kodi Yehova sali pakati pa ife? palibe coipa codzatigwera.