Micah 3:2 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mumadana ndi zabwino, mumakonda zoipa. Anthu anga mumaŵasenda amoyo, ndi kukangadzula mnofu wao.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Inu amene mudana nacho chokoma ndi kukondana nacho choipa; inu akumyula khungu lao pathupi pao, ndi mnofu wao pa mafupa ao;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
inu amene mumadana ndi zabwino ndi kukonda zoyipa; inu amene mumasenda khungu la anthu anga, ndipo mumakungunula mnofu pa mafupa awo;
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
inu amene mudana naco cokoma ndi kukondana naco coipa; inu akumyula khungu lao pathupi pao, ndi mnofu wao pa mafupa ao;