Micah 3:4 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Nthaŵi ikubwera pamene mudzalira kwa Chauta, koma sadzakuyankhani. Nthaŵi imeneyo adzakufulatirani chifukwa ntchito zanu nzoipa.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo adzafuulira kwa Yehova, koma sadzawayankha; inde, adzawabisira nkhope yake nthawi yomweyo, monga momwe anaipsa machitidwe ao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pamenepo adzalira kwa Yehova, koma Iye sadzawayankha. Nthawi imeneyo Iye adzawabisira nkhope yake chifukwa cha zoyipa zimene anazichita.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo adzapfuulira kwa Yehova, koma sadzawayankha; inde, adzawabisira nkhope yace nthawi yomweyo, monga momwe anaipsa macitidwe ao.