Micah 3:5 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Zimene akunena Chauta ndi izi: “Pali aneneri amene amasokeza anthu anga: amamlosera za mtendere amene amaŵadyetsa, koma amamlosera nkhondo amene alibe choŵapatsa.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Atero Yehova za aneneri akulakwitsa anthu anga; akuluma ndi mano ao, ndi kufuula, Mtendere; ndipo aliyense wosapereka m'kamwa mwao, amkonzera nkhondo;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yehova akuti, “Aneneri amene amasocheretsa anthu anga, ngati munthu wina awapatsa chakudya amamufunira ‘mtendere;’ ngati munthu wina sawapatsa zakudya amamulosera zoyipa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Atero Yehova za aneneriakulakwitsa anthu anga; akuluma ndi mano ao, ndi kupfuula, Mtendere; ndipo, ali yense wosapereka m'kamwa mwao, amkonzera nkhondo;