Micah 3:8 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma ine Chauta wandidzaza ndi mphamvu, wandidzaza ndi mzimu wake. Wandidzaza ndi kulungama ndi kulimba mtima, kuti ndidzudzule a banja la Yakobe chifukwa cha zolakwa zao, kuti ndiwonetse Aisraele zoipa zao.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma ine ndidzala nayo mphamvu mwa Mzimu ya Yehova, ndi chiweruzo, ndi chamuna, kufotokozera Yakobo kulakwa kwake, ndi kwa Israele tchimo lake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma kunena za ine, ndadzazidwa ndi mphamvu, ndi Mzimu wa Yehova, ndi kulungama, ndi kulimba mtima, kuti ndilalikire za kugalukira kwa Yakobo, kwa Israeli za tchimo lake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma ine ndidzala nayo mphamvu mwa Mzimu ya Yehova, ndi ciweruzo, ndi camuna, kufotokozera Yakobo kulakwa kwace, ndi kwa Israyeli cimo lace.