Micah 4:10 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Muphiriphithe ndi kubuula, inu anthu a ku Ziyoni, ngati mkazi pa nthaŵi yake yochira. Pakuti tsopano mudzachoka mumzindamo, mukakhala mumidzi. Mudzachotsedwa kupita ku Babiloni. Komabe kumeneko mudzapulumutsidwa, kumeneko Chauta adzakuwombolani kwa adani anu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Imva zowawa, nuyesetse kubala, mwana wamkazi wa Ziyoni, ngati mkazi wakubala; pakuti udzatuluka m'mudzi tsopano, nudzakhala kuthengo, nudzafika ku Babiloni; komweko udzapulumutsidwa; komweko Yehova adzakuombola m'manja a adani ako.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Gubuduka ndi ululu, iwe mwana wamkazi wa Ziyoni, ngati mayi pa nthawi yake yobereka, pakuti tsopano muyenera kuchoka mu mzinda ndi kugona kunja kwa mzindawo. Udzapita ku Babuloni; kumeneko udzapulumutsidwa, kumeneko Yehova adzakuwombola mʼmanja mwa adani ako.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Imva zowawa, nuyesetse kubala, mwana wamkazi wa Ziyoni, ngati mkazi wakubala; pakuti udzaturuka m'mudzi tsopano, nudzakhala kuthengo, nudzafika ku Babulo; komweko udzapulumutsidwa; komweko Yehova adzakuombola m'manja a adani ako.