Micah 4:13 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Yamba kupuntha iwe Ziyoni, ndidzakusandutsa wamphamvu ngati nkhunzi ya nyanga zachitsulo, ngati nkhunzi ya ziboda zamkuŵa. Udzatswanya mitundu yambiri ya anthu, zimene adapindula udzazipereka kwa Chauta, chuma chao udzachipereka kwa Ambuye a dziko lonse lapansi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Nyamuka nupunthe, mwana wamkazi wa Ziyoni; pakuti ndidzasanduliza nyanga yako ikhale yachitsulo, ndi ziboda zako zikhale zamkuwa; ndipo udzaphwanya mitundu yambiri ya anthu; ndipo uzipereka chiperekere phindu lao kwa Yehova, ndi chuma chao kwa Ambuye wa dziko lonse lapansi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Imirira, puntha, iwe mwana wamkazi wa Ziyoni, pakuti ndidzakupatsa nyanga zachitsulo; ndidzakupatsa ziboda zamkuwa ndipo udzaphwanya mitundu yambiri ya anthu.” Phindu lawo lolipeza molakwikalo udzalipereka kwa Yehova, chuma chawo kwa Yehova wa dziko lonse lapansi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Nyamuka nupunthe, mwana wamkazi wa Ziyoni; pakuti ndidzasanduliza nyanga yako ikhale yacitsulo, ndi ziboda zako zikhale zamkuwa; ndipo udzaphwanya mitundu yambiri ya anthu; ndipo uzipereka ciperekere phindu lao kwa Yehova, ndi cuma cao kwa Ambuye wa dziko lonse lapansi.