Micah 4:3 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Iyeyo adzaweruza pakati pa mitundu yambiri ya anthu, adzathetsa kusamvana pakati pa mafuko amphamvu, ngakhale akutali omwe. Anthuwo adzasula malupanga ao kuti akhale makasu, ndiponso mikondo yao kuti ikhale mapwitika. Mitundu ya anthu sidzasamulirananso malupanga, sidzaphunziranso zomenyana nkhondo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Iye adzaweruza mwa mitundu yambiri ya anthu, nadzadzudzula amitundu amphamvu ali kutali; ndipo iwo adzasula malupanga ao akhale makasu, ndi mikondo yao ikhale zolimira, mtundu wa anthu sudzasamulira mtundu unzake lupanga, kapena kuphunziranso nkhondo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iye adzaweruza pakati pa anthu amitundu yambiri ndipo adzathetsa kusamvana pakati pa anthu amphamvu akutali ndi apafupi omwe. Anthuwo adzasandutsa malupanga awo kukhala makasu ndiponso mikondo yawo kukhala zomwetera. Mtundu wina sudzatenganso lupanga kumenyana ndi mtundu wina, kapena kuphunziranso za nkhondo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Iye adzaweruza mwa mitundu yambiri ya anthu, nadzadzudzula amitundu amphamvu ali kutali; ndipo iwo adzasula malupanga ao akhale makasu, ndi mikondo yao ikhale mazenga, mtundu wa anthu sudzasamulira mtundu unzace lupanga, kapena kuphunziranso nkhondo.