Micah 4:8 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Tsono iwe Ziyoni, nsanja yotetezera nkhosa zanga, phiri la anthu anga, zimene ndidaakulonjeza zidzachitikadi. Ufumu wako wakale uja udzakubwereranso, Anthu a ku Yerusalemu ufumu wao uja udzafikanso.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo iwe, nsanja ya nkhosa, chitunda cha mwana wamkazi wa Ziyoni, udzafikira iwe, inde udzafika ulamuliro wakale, ufumu wa mwana wamkazi wa Yerusalemu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kunena za iwe, nsanja ya ziweto zanga, iwe linga la mwana wamkazi wa Ziyoni, ulamuliro wako wakale udzabwezeretsedwa kwa iwe; ufumu udzabwera pa mwana wamkazi wa Yerusalemu.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo iwe, nsanja ya nkhosa, citunda ca mwana wamkazi wa Ziyoni, udzafikira iwe, inde udzafika ulamuliro wakale, ufumu wa mwana wamkazi wa Yerusalemu.