Micah 4:9 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kodi ukuliriranji mokuŵa chonchi mzinda iwe? Ukusaukiranji ngati mkazi pa nthaŵi yake yochira? Kodi ndiye kuti ulibe mfumu, kapena phungu wokulangiza?
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Tsono ufuulitsa chifukwa ninji? Palibe mfumu mwa iwe kodi? Watayika kodi mu uphungu wako, kuti zowawa zakugwira ngati mkazi wobala?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Chifukwa chiyani tsopano ukulira mofuwula, kodi ulibe mfumu? Kodi phungu wako wawonongedwa, kotero kuti ululu wako uli ngati wa mayi amene akubereka?
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Tsono upfuulitsa cifukwa ninji? palibe mfumu mwa iwe kodi? watayika kodi mu uphungu wako, kuti zowawa zakugwira ngati mkazi wobala?