Micah 5:13 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndidzaononga mafano anu onse pamodzi ndi miyala yoimika yopembedzerapo m'dziko mwanu. Simudzazigwadiranso zinthuzo zimene mudapanga ndi manja anu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndidzaononganso mafano ako osema, ndi zoimiritsa zako pakati pako; ndipo sudzalambiranso ntchito za manja ako.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndidzawononga mafano anu osema pamodzi ndi miyala yanu yopatulika imene ili pakati panu; simudzagwadiranso zinthu zopanga ndi manja anu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndidzaononganso mafano ako osema, ndi zoimiritsa zako pakati pako; ndipo sudzalambiranso nchito za manja ako.