Micah 5:2 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chauta akuti, “Koma iwe Betelehemu wa ku Efurata, inde ndiwe wamng'ono pakati pa mafuko a Yuda, komabe mwa iwe ndidzatulutsa munthu amene adzakhala wolamulira Israele. Iyeyo chiyambi chake nchakalekale, cha masiku amakedzana.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma iwe, Betelehemu Efurata, ndiwe wamng'ono kuti ukhale mwa zikwi za Yuda, mwa iwe mudzanditulukira wina wakudzakhala woweruza m'Israele; matulukiro ake ndiwo a kale lomwe, kuyambira nthawi yosayamba.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Koma iwe Betelehemu Efurata, ngakhale uli wonyozeka pakati pa mafuko a Yuda, mwa iwe mudzatuluka munthu amene adzalamulira Israeli, amene chiyambi chake nʼchakalekale, nʼchamasiku amakedzana.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma iwe, Betelehemu Efrata, ndiwe wamng'ono kuti ukhale mwa zikwi za Yuda, mwa iwe mudzanditurukira wina wakudzakhala woweruza m'Israyeli; maturukiro ace ndiwo a kale lomwe, kuyambira nthawi yosayamba.