Micah 5:3 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nchifukwa chake Mulungu adzasiya Israele mpaka pa nthaŵi yoti achire mkazi amene adzabale mwana. Pamenepo, otsala a mtundu wake adzabwereranso kwa Aisraele anzao.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chifukwa chake Iye adzawapereka kufikira nthawi yoti wobalayo wabala; pamenepo otsala a abale ake adzabwera pamodzi ndi ana a Israele.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Nʼchifukwa chake Israeli adzasiyidwa mpaka pa nthawi imene mayi amene ali woyembekezera adzachire. Ndipo abale ake onse otsalira adzabwerera kudzakhala pamodzi ndi Aisraeli.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cifukwa cace Iye adzawapereka kufikira nthawi yoti wobalayo wabala; pamenepo otsala a abale ace adzabwera pamodzi ndi ana a Israyeli,