Micah 5:6 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Iwowo adzagonjetsa dziko la Asiriya ndi lupanga, dziko la Nimirodi adzalilamulira mwankhondo. Adzatipulumutsa kwa Aasiriya, iwowo akadzakaloŵa m'dziko mwathu, kudzatithira nkhondo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo iwo adzatha dziko la Asiriya ndi lupanga, ndi dziko la Nimirodi, ndilo polowera pake; ndipo adzatilanditsa kwa a ku Asiriya pamene alowa m'dziko lathu, pamene aponda m'kati mwa malire athu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iwo adzagonjetsa dziko la Asiriya ndi lupanga, dziko la Nimurodi adzalilamulira mwankhondo. Adzatipulumutsa kwa Asiriya akadzafika mʼmalire a mʼdziko lathu kudzatithira nkhondo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo iwo adzatha dziko la Asuri ndi lupanga, ndi dziko la Nimrodi, ndilo polowera pace; ndipo adzatilanditsa kwa a ku Asuri pamene alowa m'dziko lathu, pamene aponda m'kati mwa malire athu.