Micah 5:7 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Onse otsalira a Yakobe adzakhala dalitso pakati pa mitundu yambiri ya anthu ngati mame ochoka kwa Chauta. Adzakhala ngati mvula yowaza pa udzu, imene sichita kulamulidwa ndi anthu, siidikira lamulo la munthu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo otsala a Yakobo adzakhala pakati pa mitundu yambiri ya anthu, ngati mame ochokera kwa Yehova ngati mvula paudzu, yosachedwera munthu, yosalindira ana a anthu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Otsalira a Yakobo adzakhala pakati pa mitundu yambiri ya anthu ngati mame ochokera kwa Yehova, ngati mvumbi pa udzu, omwe sulamulidwa ndi munthu kapena kudikira lamulo la anthu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo otsala a Yakobo adzakhala pakati pa mitundu yambiri ya anthu, ngati mame ocokera kwa Yehova, ngati mvula paudzu, yosacedwera munthu, yosalindira ana a anthu.