Micah 5:8 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Onse otsalira a Yakobe adzakhala temberero pakati pa mitundu ya anthu, ngati mkango pakati pa nyama zam'nkhalango. Adzakhala ngati mwana wa mkango, pakati pa gulu la nkhosa, amene amati akadzaziloŵerera, amazimbwandira ndi kuzikadzula. Ndipo sipakhala wozipulumutsa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo otsala a Yakobo adzakhala mwa amitundu, pakati pa mitundu yambiri ya anthu, ngati mkango mwa nyama zakuthengo, ngati msona wa mkango mwa magulu a nkhosa; umenewo ukapitako, upondereza, numwetula, ndipo palibe wakupulumutsa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Otsala a Yakobo adzakhala pakati pa mitundu ya anthu, mʼgulu la anthu a mitundu yambiri, ngati mkango pakati pa nyama za mʼnkhalango. Ngati mwana wa mkango pakati pa gulu la nkhosa, amene pozidutsa amazidya ndi kuzikhadzula, ndipo palibe angathe kuzilanditsa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo, otsala a Yakobo adzakhala mwa amitundu, pakati pa mitundu yambiri ya anthu, ngati mkango mwa nyama za kuthengo, ngati msona wa mkango mwa magulu a nkhosa; umenewo ukapitako, upondereza, numwetula, ndipo palibe wakupulumutsa.