Micah 6:16 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mwasunga machitidwe oipa a mfumu Omuri ndi ntchito zonse za banja la Ahabu. Mwatsata njira zao zonse. Motero ndidzakuwonongani kotheratu. Anthu a mitundu ina adzakunyodolani, kulikonse anthu adzakunyozani.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti asunga malemba a Omuri, ndi ntchito za nyumba ya Ahabu, ndipo mumayenda m'uphungu wao; kuti ndikusandulize bwinja, ndi okhalamo chotsonya; ndipo mudzasenza chitonzo cha anthu anga.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Inu mwatsatira malangizo a Omuri ndiponso machitidwe onse a banja la Ahabu, ndi khalidwe lawo lonse. Choncho Ine ndidzakuperekani kuti muwonongedwe ndiponso anthu anu kuti azunguzike mitu; mudzanyozedwa ndi anthu a mitundu ina.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti asunga malemba a Omri, ndi nchito za nyumba ya Ahabu, ndipo mumayenda m'uphungu wao; kuti ndikusandulize bwinja, ndi okhalamo cotsonya; ndipo mudzasenza citonzo ca anthu anga.