Micah 6:2 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Imvani mlandu wa Chauta, inu mapiri, ndi inunso maziko amuyaya a dziko lapansi. Chautatu akuimba mlandu anthu ake, akutsutsana ndi Aisraele.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Tamverani, mapiri inu, chitsutsano cha Yehova, ndi inu maziko olimba a dziko lapansi; pakuti Yehova ali nacho chitsutsano ndi anthu ake, ndipo adzatsutsana ndi Israele.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Imvani mlandu wa Yehova, inu mapiri; tamverani, maziko amuyaya a dziko lapansi. Pakuti Yehova ali ndi mlandu ndi anthu ake; Iye akutsutsa Aisraeli.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Tamvani, mapiri inu, citsutsano ca Yehova, ndi inu maziko olimba a dziko lapansi; pakuti Yehova ali naco citsutsano ndi anthu ace, ndipo adzatsutsana ndi Israyeli.