Micah 6:4 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Paja Ine ndidakutulutsani ku dziko la Ejipito. Ndidakuwombolani ku dziko laukapololo. Ndipo ndidaachita kutuma Mose, Aroni ndi Miriyamu kuti akutsogolereni.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti ndinakukwezani kukutulutsani m'dziko la Ejipito, ndi kuombola inu m'nyumba ya ukapolo; ndipo ndinatuma akutsogolereni Mose, Aroni, ndi Miriyamu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ine ndinakutulutsani ku dziko la Igupto ndi kukuwombolani ku nyumba ya ukapolo. Ndinatuma Mose kuti akutsogolereni, pamodzi ndi Aaroni ndi Miriamu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti ndinakukwezani kukuturutsani m'dziko la Aigupto, ndi kuombola inu m'nyumba ya ukapolo; ndipo ndinatuma akutsogolereni Mose, Aroni, ndi Miriamu.