Micah 6:5 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Inu anthu anga, kumbukirani zimene Balaki, mfumu ya ku Mowabu, adaafuna kukuchitani, ndiponso m'mene Balamu mwana wa Beori adamuyankhira. Kumbukirani zimene zidachitika pa ulendo wochoka ku Sitimu kupita ku Giligala. Kumbukirani zonsezi kuti muzindikire zimene Ine Chauta ndidachita pofuna kukupulumutsani.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Anthu anga, kumbukiranitu chofunsira Balaki mfumu ya Mowabu, ndi chomuyankha Balamu mwana wa Beori, kuyambira ku Sitimu kufikira ku Giligala; kuti mudziwe zolungama za Yehova.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anthu anga, kumbukirani zimene Balaki mfumu ya ku Mowabu inafuna kukuchitirani ndiponso zimene Balaamu mwana wa Beori anayankha. Kumbukirani zomwe zinachitika pa ulendo wochoka ku Sitimu kupita ku Giligala, kuti mudziwe machitidwe olungama a Yehova.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Anthu anga, kumbukilanitu cofunsira Balaki mfumu ya Moabu, ndi comuyankha Balamu mwana wa Beori, kuyambira ku Sitimu kufikira ku Giligala; kuti mudziwe zolungama za Yehova.