Micah 6:7 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kodi Chauta adzakondwera ndi nkhosa zamphongo zikwi zingapo kapena mitsinje ya mafuta zikwi khumi? Kodi ndidzapereke mwana wanga wachisamba chifukwa cha zolakwa zanga? Kodi mwana wanga adzakhale nsembe yolipira tchimo langa?
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Kodi Yehova adzakondwera nazo nkhosa zamphongo zikwi, kapena ndi mitsinje ya mafuta zikwi khumi? Kodi ndipereke mwana wanga woyamba chifukwa cha kulakwa kwanga, chipatso cha thupi langa chifukwa cha kuchimwa kwa moyo wanga?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kodi Yehova adzakondwera ndi nkhosa zazimuna 1,000, kapena ndi mitsinje yosalekeza ya mafuta? Kodi ndipereke nsembe mwana wanga woyamba kubadwa chifukwa cha zolakwa zanga? Chipatso cha thupi langa chifukwa cha tchimo la moyo wanga?
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Kodi Yehova adzakondwera nazo nkhosa zamphongo zikwi, kapena ndi mitsinje ya mafuta zikwi khumi? Kodi ndipereke mwana wanga woyamba cifukwa ca kulakwa kwanga, cipatso ca thupi langa cifukwa ca kucimwa kwa moyo wanga?