Micah 7:1 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kalanga ine! Ndasanduka ngati wokunkha wosapeza zotsalira. Sipadatsalenso mphesa zoti nkudya. Sipadatsaleko nkhuyu zimene ndimazikonda.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Kalanga ine! Pakuti ndikunga atapulula zipatso za m'mwamvu, atakunkha m'munda wamphesa; palibe mphesa zakudya; moyo wanga ukhumba nkhuyu yoyamba kupsa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsoka ine! Ndili ngati munthu wokunkha zipatso nthawi yachilimwe, pa nthawi yokolola mphesa; palibe phava lamphesa loti nʼkudya, palibe nkhuyu zoyambirira zimene ndimazilakalaka kwambiri.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Kalanga ine! pakuti ndikunga atapulula zipatso za m'mwamvu, atakunkha m'munda wamphesa; palibe mphesa zakudya; moyo wanga ukhumba nkhuyu yoyamba kupsa.