Micah 7:10 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono adani athu adzaona zimenezi, ndipo manyazi adzaŵagwira anthu amene ankatifunsa kuti, “Ali kuti Chauta, Mulungu wanu?” Tidzaona kugonjetsedwa kwao, adzaponderezedwa ngati matope m'miseu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo mdani wanga adzachiona, ndi manyazi adzamkuta iye amene adati kwa ine, Ali kuti Yehova Mulungu wako? Maso anga adzamuona; tsopano adzampondereza ngati thope la m'miseu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo mdani wanga adzaona zimenezi nadzagwidwa ndi manyazi, iye amene anandifunsa kuti, “Ali kuti Yehova Mulungu wako?” Ndidzaona kugonjetsedwa kwake ndi maso anga; ngakhale tsopano adzaponderezedwa ngati matope mʼmisewu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo mdani wanga adzaciona, ndi manyazi adzamkuta iye amene adati kwa ine, Ali kuti Yehova Mulungu wako? Maso anga adzamuona; tsopano adzampondereza ngati thope la m'miseu.