Micah 7:12 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nthaŵi imeneyo anthu anu adzabwerera kwa inu kuchokera ku Asiriya mpaka ku Ejipito, kuchokera ku Ejipito mpaka ku Mtsinje wa Yufurate, ndiponso kuchokera ku nyanja ina mpaka ku nyanja inanso, kuchokera ku phiri lina mpaka ku phiri linanso.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Tsiku lomwelo adzadza kwa iwe, kuchokera ku Asiriya ndi midzi ya ku Ejipito, kuyambira ku Ejipito kufikira ku Mtsinje, ndi kuyambira kunyanja kufikira kunyanja, ndi kuyambira kuphiri kufikira kuphiri.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Nthawi imeneyo anthu adzabwera kwa inu kuchokera ku Asiriya ndi mizinda ya ku Igupto, ngakhale kuchokera ku Igupto mpaka ku Yufurate ndiponso kuchokera ku nyanja ina mpaka ku nyanja inanso kuchokera ku phiri lina mpaka ku phiri linanso.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Tsiku lomwelo adzadza kwa iwe, kucokera ku Asuri ndi midzi ya ku Aigupto, kuyambira ku Aigupto kufikira ku Mtsinje, ndi kuyambira kunyanja kufikira kunyanja, ndi kuyambira kuphiri kufikira kuphiri.