Micah 7:14 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Inu Chauta muŵatsogolere anthu anu ndi ndodo yanu yoŵatetezera, muŵete nkhosa zanu zimene mudazisankha. Tsopano zikukhala zokha m'nkhalango pakati pa dziko la chonde. Koma muzilole kuti zikadye ku busa labwino, ku Basani ndi Giliyadi, monga masiku akale.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mudyetse anthu anu ndi ndodo yanu, nkhosa za cholowa chanu zokhala pa zokha m'nkhalango pakati pa Karimele, zidye m'Basani ndi m'Giliyadi masiku a kale lomwe.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Wetani anthu anu ndi ndodo yanu yowateteza, nkhosa zimene ndi cholowa chanu, zimene zili zokha mʼnkhalango, mʼdziko la chonde. Muzilole kuti zidye mu Basani ndi mu Giliyadi monga masiku akale.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mudyetse anthu anu ndi ndodo yanu, nkhosa za colowa canu zokhala pa zokha m'nkhalango pakati pa Karimeli, zidye m'Basana ndi m'Gileadi masiku a kale lomwe.