Micah 7:16 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Anthu a mitundu yambiri akadzaona zimenezo adzachita manyazi, ngakhale ali ndi mphamvu zotani. Adzangogwira pakamwa, ndi kutseka makutu motaya mtima.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Amitundu adzaona nadzachita manyazi ndi mphamvu yao yonse; adzagwira pakamwa, m'makutu mwao mudzagontha.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mitundu ya anthu idzaona zimenezi ndipo idzachita manyazi, ngakhale ali ndi mphamvu zotani. Adzagwira pakamwa pawo ndipo makutu awo adzagontha.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Amitundu adzaona nadzacita manyazi ndi mphamvu yao yonse; adzagwira pakamwa, m'makutu mwao mudzagontha.