Micah 7:17 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adzavimvinizika pa dothi ngati njoka, ngati zolengedwa zina zokwaŵa. Adzabwera ali njenjenje kuchokera ku malinga ao. Moopa adzatembenukira kwa Inu Chauta, Mulungu wathu, ndipo adzachita nanu mantha.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Adzanyambita fumbi ngati njoka; ngati zokwawa za padziko, adzanjenjemera potuluka m'ngaka mwao; adzafika kwa Yehova Mulungu wao ndi mantha, nadzaopa chifukwa cha iwe.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Adzabwira fumbi ngati njoka, ngati zolengedwa zomwe zimakwawa pansi. Adzabwera akunjenjemera kuchokera mʼmaenje awo; mwamantha adzatembenukira kwa Yehova Mulungu wathu ndipo adzachita nanu mantha.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Adzanyambita pfumbi ngati njoka; ngati zokwawa za padziko, adzanjenjemera poturuka m'ngaka mwao; adzafika kwa Yehova Mulungu wao ndi mantha, nadzaopa cifukwa ca iwe.