Micah 7:18 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kodi ndani ali Mulungu ngati Inu, amene amakhululukira machimo ndi kuiŵala zolakwa za anthu anu otsala? Simusunga mkwiyo mpaka muyaya, chifukwa muli ndi chikondi chosasinthika.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndani Mulungu wofanana ndi Inu, wakukhululukira mphulupulu, wakupitirira zolakwa za otsala a cholowa chake? Sasunga mkwiyo wake kunthawi yonse popeza akondwera nacho chifundo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kodi alipo Mulungu wofanana nanu, amene amakhululukira tchimo ndi kuyiwala zolakwa za anthu otsala amene ndi cholowa chake? Inu simusunga mkwiyo mpaka muyaya koma kwanu nʼkuonetsa chikondi chosasinthika.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndani Mulungu wofanana ndi Inu, wakukhululukira mphulupulu, wakupitirira zolakwa za otsala a colowa cace? sasunga mkwiyo wace ku nthawi yonse popeza akondwera naco cifundo.