Micah 7:3 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndi akatswiri pochita zoipa. Akalonga ndi aweruzi amafuna ziphuphu, ndipo mtsogoleri amaŵauza zoipa zimene afuna kuti iwo achite. Motero amalakwira pamodzi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Manja ao onse awiri agwira choipa kuchichita ndi changu; kalonga apempha, ndi woweruza aweruza chifukwa cha mphotho; ndi wamkuluyo angonena chosakaza moyo wake; ndipo achiluka pamodzi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Manja awo onse ndi aluso pochita zoyipa; wolamulira amafuna mphatso, woweruza amalandira ziphuphu, anthu amphamvu amalamula kuti zichitike zimene akuzifuna, onse amagwirizana zochita.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Manja ao onse awiri agwira coipa kucicita ndi cangu; kalonga apempha, ndi woweruza aweruza cifukwa ca mphotho; ndi wamkuruyo angonena cosakaza moyo wace; ndipo aciluka pamodzi.