Micah 7:6 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Makono ana aamuna akunyoza atate ao, ana aakazi akuukira amai ao. Mtengwa akulongolozana ndi mpongozi wake, nkhondo ndi anansi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti mwana wamwamuna apeputsa atate, mwana wamkazi aukira amake, mpongozi aukira mpongozi wake; adani ake a munthu ndiwo a m'nyumba yake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pakuti mwana wamwamuna akunyoza abambo ake, mwana wamkazi akuwukira amayi ake, mtengwa akukangana ndi apongozi ake, adani a munthu ndi amene amakhala nawo mʼbanja mwake momwe.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti mwana wamwamuna apeputsa atate, mwana wamkazi aukira amace, mpongozi aukira mpongozi wace; adani ace a munthu ndiwo a m'nyumba yace.