Micah 7:9 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tachimwira Chauta, nchifukwa chake tiyenera kupirira mkwiyo wake, mpaka atazenga mlandu wathu ndi kuugamula. Koma pambuyo pake adzatiloŵetsa m'kuŵala, ndipo tidzaona chipulumutso chake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndidzasenza mkwiyo wa Yehova, chifukwa ndamchimwira, mpaka andinenera mlandu wanga, ndi kundiweruzira mlandu wanga; adzanditulutsira kwa kuunika, ndipo ndidzapenya chilungamo chake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndidzapirira mkwiyo wa Yehova, chifukwa ndinamuchimwira, mpaka ataweruza mlandu wanga ndi kukhazikitsa chilungamo changa. Iye adzanditulutsa ndi kundilowetsa mʼkuwunika; ndidzaona chilungamo chake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndidzasenza mkwiyo wa Yehova, cifukwa ndamcimwira, mpaka andinenera mlandu wanga, ndi kundiweruzira mlandu wanga; adzanditurutsira kwa kuunika, ndipo ndidzapenya cilungamo cace.