Nahum 1:12 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Zimene akunena Chauta ndi izi, akuti, “Ngakhale Aasiriyawo ndi amphamvu ndiponso ndi ambiri, adzaonongeka ndi kutheratu. Koma inu anthu anga, ngakhale ndidakulangani, sindidzakulanganinso.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Atero Yehova: Angakhale iwo ali ndi mphamvu yokwanira, nachuluka momwemo, koma momwemonso adzasalikidwa, ndipo iye adzapitiratu. Chinkana ndakuzunza iwe, sindidzakuzunzanso.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yehova akuti, “Ngakhale Asiriyawo ali ndi abwenzi, kaya iwowo ndi ambiri, koma adzawonongedwa ndi kutheratu. Ngakhale ndinakuzunza iwe Yuda, sindidzakuzunzanso.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Atero Yehova: Angakhale iwo ali ndi mphamvu yokwanira, nacuruka momwemo, koma momwemonso adzasalikidwa, ndipo iye adzapitiratu. Cinkana ndakuzunza iwe, sindidzakuzunzanso.