Nahum 1:14 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Za inu a ku Ninive Chauta walamula kuti, “Simudzakhala ndi adzukulu otchedwa dzina lanu. Ndidzaononga mafano osema ndi oumba m'nyumba ya milungu yanu. Ndidzakukumbirani manda, chifukwa ndinu opandapake.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Yehova walamulira za iwe kuti asabzalidwenso ena a dzina lako; m'nyumba ya milungu yako ndidzachotsa fano losema ndi fano loyenga; ndidzakukonzerapo manda, pakuti iwe ndiwe wopepuka.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yehova walamulira za iwe, Ninive kuti, “Sudzakhala ndi zidzukulu zimene zidzadziwike ndi dzina lako. Ndidzawononga zifanizo zosema ndi mafano owumba amene ali mʼnyumba ya milungu yako. Ine ndidzakukumbira manda chifukwa ndiwe woyipitsitsa.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Yehova walamulira za iwe kuti asabzalidwenso ena a dzina lako; m'nyumba ya milungu yako ndidzacotsa fano losema ndi fano loyenga; ndidzakukonzerapo manda, pakuti iwe ndiwe wopepuka.