Nahum 1:3 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chauta ndi wamphamvu zedi. Ndi wosakwiya msanga, komabe sadzalola kuti munthu wochimwa akhale wosalangidwa. Pamene amayenda pamachitika kamvulumvulu ndi mphepo yamkuntho, mitambo ndiye fumbi limene mapazi ake amachititsa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Yehova ndiye wolekerera mkwiyo, koma wa mphamvu yaikulu; ndi wosamasula ndithu wopalamula; njira ya Yehova ili m'kamvulumvulu ndi mumkuntho; ndipo mitambo ndiyo fumbi la mapazi ake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yehova sakwiya msanga koma ndi wa mphamvu yayikulu; ndipo sadzalola kuti munthu wolakwa asalangidwe. Iye amayenda mʼkamvuluvulu ndi mʼnamondwe, ndipo mitambo ndi fumbi la ku mapazi ake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Yehova ndiye wolekerera mkwiyo, koma wa mphamvu yaikuru; ndi wosamasula ndithu woparamula; njira ya Yehova iri m'kabvumvulu ndi mumkuntho; ndipo mitambo ndiyo pfumbi la mapazi ace.