Nahum 1:5 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mapiri amagwedezeka pamaso pake, magomo amasungunuka. Dziko lapansi limanjenjemera pamaso pake, ndiye kuti dziko ndi zonse zokhala m'menemo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mapiri agwedezeka chifukwa cha Iye, ndi zitunda zisungunuka; ndi dziko lapansi likwezeka pamaso pake, ndi maiko ndi onse okhala m'mwemo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mapiri amagwedera pamaso pake ndipo zitunda zimasungunuka. Dziko lapansi limanjenjemera pamaso pake, dziko lonse ndi zonse zokhala mʼmenemo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mapiri agwedezeka cifukwa ca Iye, ndi zitunda zisungunuka; ndi dziko lapansi likwezeka pamaso pace, ndi maiko ndi onse okhala m'mwemo.