Nahum 1:6 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kodi ndani angathe kuima pamaso pa Chauta, Iye atakwiya? Kodi ndani angathe kupirira ukali wake? Ukali wake umayaka ngati moto, matanthwe amadyukuka pamaso pake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Adzaima ndani pa kulunda kwake? Ndipo adzakhalitsa ndani pa mkwiyo wake wotentha? Ukali wake utsanulidwa ngati moto, ndi matanthwe asweka ndi Iye.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndani angathe kuyima pamaso pake Iye akalusa? Ndani angapirire mkwiyo wake woopsa? Ukali wake ukuyaka ngati moto; matanthwe akunyeka pamaso pake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Adzaima ndani pa kulunda kwace? ndipo adzakhalitsa ndani pa mkwiyo wace wotentha? ukali wace utsanulidwa ngati moto, ndi matanthwe asweka ndi Iye.