Nahum 2:11 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kodi tsopano mzinda uja uli kuti? Unali ngati phanga la mikango, m'mene ana ake ankadyeramo, m'mene mikango yonse inkakhala mopanda mantha.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ili kuti ngaka ya mikango, ndi podyera misona ya mikango, kumene mkango, waumuna ndi waukazi, ukayenda ndi mwana wa mkango, kopanda wakuiposa?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kodi tsopano dzenje la mikango lili kuti, malo amene mikango inkadyetserako ana ake, kumene mkango waumuna ndi waukazi unkapitako, ndipo ana a mkango sankaopa kanthu kalikonse?
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Iri kuti ngaka ya mikango, ndi podyera misona ya mikango; kumene mkango, waumuna ndi waukazi, ukayenda ndi mwana wa mkango, kopanda wakuiposa?