Nahum 2:12 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mkango wamphongo unkapha nyama yokwanira mkango waukazi ndi ana ake. Unkadzaza phanga lakelo ndi nyama yokadzulakadzula.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mkangowo unamwetula zofikira ana ake, nusamira yaikazi yake, nudzaza mapanga ake ndi nyama, ngaka zake ndi zojiwa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mkango waumuna unkapha nyama yokwanira ana ake ndiponso kuphera nyama mkango waukazi, kudzaza phanga lake ndi zimene wapha ndiponso dzenje lake ndi nyama imene waphayo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mkangowo unamwetula zofikira ana ace, nusamira yaikazi yace, nudzaza mapanga ace ndi nyama, ngaka zace ndi zojiwa.