Nahum 2:13 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chauta Wamphamvuzonse akuuza a ku Ninive kuti, “Ine sindikugwirizana nanu, ndidzakutentherani magaleta anu. Lupanga lidzakuwonongerani ankhondo anu amene ali ngati mikango. Ndidzakulandani zonse zimene mudafunkha pa dziko lapansi. Amithenga anu sadzamvekanso mau.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Taona, nditsutsana nawe, ati Yehova wa makamu, ndipo ndidzatentha magaleta ake m'utsi; ndi lupanga lidzadya misona yako ya mkango; ndipo ndidzachotsa zofunkha zako pa dziko lapansi, ndi mau a mithenga yako sadzamvekanso.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yehova Wamphamvuzonse akuti, “Ine ndikutsutsana nawe. Ndidzatentha magaleta ako mpaka utsi tolotolo, ndipo lupanga lidzapha mikango yako yayingʼono; sindidzakusiyira chilichonse choti udye pa dziko lapansi. Mawu a amithenga anu sadzamvekanso.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Taona, nditsutsana nawe, ati Yehova wa makamu, ndipo ndidzatentha magareta ace m'utsi; ndi lupanga lidzadya misona yako ya mkango; ndipo ndidzacotsa zofunkha zako pa dziko lapansi, ndi mau a mithenga yako sadzamvekanso.